Katswiri pa nkhani za malamulo a Justine Dzonzi anena kuti m’dziko muno mudzakhala chipwirikiti ngati chisankho Cha chibweleza Cha pulezidenti chilephereke kuchitika pakatha masiku 150 malingana ndi chigamulo Cha Khothi la malamulo.
Katswiriyu wanena kuti nyumba ya malamulo ikuyenera kukhazikitsa tsiku lochititsira chisankho chachibwereza Cha pulezidenti ndipo iye wati masiku 150 omwe Khothi linapereka azatha pa 2 July 2020 ndipo ngati chisankho chingalephereke kapena kuchedwa ndiye kuti kuyambila pa 2 July 2020 dziko lino lidzakhala lopanda pulezidenti kamba koti Prof Peter Munthalika ndi pulezidenti wongogwilizira ndipo nthawi yake idzatha pa 2 July 2020 akatha masiku 150.
Katswiriyu wafotokoza kuti aphungu anyumbayi asatengere ndale nkhaniyi chifukwa zofuna a anthu zikuyenela kukwanisidwa potsata lamulo losankha mtsogoleri yemwe akumufuna.
Dzonzi wanenanso kuti aphunguwa apange chiganizo chomanga dziko monga Amalawi osati chopasula kamba kadyera.