Bungwe la HRDC lati lakhumudwa kwambiri ndi tsogoleri wa Kongeresi pa momwe wasankhila nduna zake.
Bungweli lati lalandila madandaulo a aMalawi ambiri omwe ndi okhumudwa ndi zomwe wachita mtsogoleriyu posankha nduna zopanda pake zomwe. Zina mwa izo ndi za banja limodzi, komanso zina zidapalamulapo m’mbuyomu milandu yosiyasiyana monga yokuba ma bed ku chipatala ndiponso zina ndi zosaphunzira komanso zochokera chigawo chimodzi cha dziko lino.
.
Bungwe la HRDC lomwe tsogoleri wake ndi Gift Trapence, lati likufuna kukumana ndi Chakwera, iwo ngati bungwe asanayambe zionesero chifukwa bungweli akuti limakhulupilira ku kambilana lisanetenge step ina. Bungweli lati kusintha zinthu komwe ankafuna anthu sikumeneku.
.
Pakadali pano anthu ambiri akhumudwa kwambiri powona Sidik Mia ndi mkazi wake komanso m’bale wake wa Mia akupasidwa unduna pomwe dziko muno muli anthu oposa 18 million.
Mwazina Chakwera wapelekaso unduna kwa munthu ndi chemwali wake, obadwa kwa Mai ndi bambo modzi. Mmbuyomu Chakwera anabwera poyela ndikuliuza dziko kuti iye saziwa kayendesedwe ka zinthu ndipo amapempha omuzungulira kuti amuthandize.
Sizikuziwika ngati ndunazi wasankha ndi Chakwera kapena omuzungulirawo.