Masiku apitawo Norman Chisale kudzera kwa anthu omuyimilira pa mlandu anakapepha ku bwalo la milandu la High Court pofuna kuti amupatse chiletso chokaniza apolisi m’dziko muno kuti asadzamumangenso iyeyo Norman Chisale pa mlandu uliwonse mtsogolomu koma bwalo la milandu la High Court linakana pempholo.
Kenako Norman Chisale anakadandawula ku bwalo la milandu la Supreme Court Of Appeal posagwilizana ndi chigamulo cha bwalo la milandu la High Court koma lero nalonso bwalo la milandu la Supreme Court Of Appeal lakana pempho la a Norman Chisale kuti asadzamamangidwenso mtsogolomu pa mlandu uliwonse womwe angadzapalamule.
Norman Chisale ndi mkulu woyang’anila chitetezo Cha mtsogoleri wakale Prof Peter Munthalika ndipo wakhala akusungidwa ku ndende kuchokera pa 14 July 2020 pa milandu itatu, woyamba wochita Katangale, wachiwiri wofuna kupha mzimayi yemwe anamuwombera ndi mfuti, wachitatu woganizilidwa kuti akukhuzidwa pa imfa ya Issa Njauju mkulu wakale wa bungwe la Ant Corruption Bureau ACB ndipo a Norman Chisale akuyenera kudzapereka pempho lawo loti atuluke pa belo pa 28 August 2020 Sabata ya mawa ndipo iwowo pakadali panopa akadali ku ndende.