Zonse zokonzekera Masewero omwe timu ya Dziko lino (The Flames ) isewere ndi timu ya Zambia masana ano zafika kumapeto izi ndi malingana ndi Mphunzitsi wa Timu ya mpira wamiyendo ya Dziko lino Meke Mwase.
Mwase wati masomphenya awo ndikukonza timu yomwe ikhale ndi kuthekera kozapambana Masewero amu Africa Cup of Nations omwe timuyi izasewere ndi timu ya Burkina Faso mwezi wa mawa.
Mwase wati ali ndi Chikuchipiliro kuti anyamata ake achita chamuna kupambana Masewero a lero ndi timu ya Zambia.
Ndipo m’mawu ake Mtsogoleri wa Osewera mu timu ya Dziko lino John Banda wayamikira Bungwe la FAM pokonza masewero apaubalewa.
CJ Banda wati limodzi ndi osewera anzake agwirizana zopambana masewerowa ndipo akudziwa bwino lomwe ubwino opambana Masewerowa malingana ndi ntchito yomwe alinayo mtsogolo muno.
Ndipo m’mawu ake yemwe watsogolera timuyi m’dziko la Zambia ( Leader of Delegation) Muhammad Selemani chomwe akudikilira ngati akulukulu omwe atsogolera timuyi ndi chipambano pamasewerowa.
Selemani wati kupambana masewerowa kuthandizira kuti Timu ya Dziko lino ikwere pa m’ndandanda wa matimu pa Dziko lonse lapansi (FIFA)