Zatsimikizika tsopano kuti Vitumbiko Kumwenda ndi mfulu moti atha kukasewera timu ina iliyonse yonse ya Ku mtima kwake kamba koti timu ya Blue Eagle yampasa chikalata (clearance).
Wanena izi ndi mlembi wa timuyi Williams Nkhoma.
Nkhoma anati iwo abwenza ndalama zokwana 3.5 million kwacha Ku timu ya silver strikers yomwe inali transfer fee yomwe anagwiriza ndipo ayibwenza kamba koti wosewerayo wakana kukasewerera timu ya silver striker.
Ndipo mkulu woyang’anira zi ntchito za silver strikers Thoko Chimbali anati Iwo abwenza chiganizo chogura vitumbiko kumwenda kamba koti wosewrayo samawonesa chidwi chosewerera timuyi ngakhale iwo anasatha njira pogura wosewerayi.
“ife ngt a silver strikers tinasatha njira yonse yoyenera pogura wosewera ndipo ndiwosewerayu tinagwirizana chilichose koma poti munthu amasintha maganizo ndy iye anawona asasainire contract ndi ife ndipo ife tangoganiza kuti tingomusiya apite timu yomwe akufuna “, anatero a Chimbali