Maiko akunja ayamikila dziko la Malawi kamba ka mtendele umene ulipo pakali pano.
Iwo anena kuti a Malawi anasankha mtsogoleli amene amkamufuna, ndipake mdziko lino muli bata ndi mtendele.
Iwo ati akuyamikila utsogoleli wathu Dr. Chakwela poyesetsa kuthandiza anthu kuti akhale ogwilizana, komaso zimene wachita posachedwapa zokaendela mtsogoleli wakale wa dziko lino professor Arthur Peter Munthalika.
Aamnenaso kuti dziko la Malawi linafika poipa kwambili, komaso chuma cha boma chinasokonekera. Koma ndi chisomo chabe kuona Dr. Chakwera akuyendetsa dziko lino ndi momwe anazipezera zinthu zitasakazika.
Ndipo ati izi zikusonyeza kuti Dr Lazarus Chakwera ali ndi kuthekera kokwanira kolamulira dziko, ngakhale anthu amene anaononga dziko lino akumafunisitsa kuwapezera zifukwa zosadziwika kuti aziti alephera mmiyezi yochepa yokha.