Chiwelengero cha anthu odwala Mlili wa Covid 19 omwe umayamba ndi kachilombo ka Corona chikunka chitsikirabe chiyambireni miyezi itatu yapitayo tsopano pomwe pa anthu 100 aliwonse, 6 ndiomwe akudwalabe.
Izi zili malingana ndi Nduna ya Zaumoyo a Kumbidze Kandodo Chiponda.
Malingana ndi Chiponda, kuchokera pa 02 April 2020 pomwe Covid inapezeka mdziko muno, mwa anthu 34, 210 omwe anapezeka nayo 32,206 achira kubweretsa chiwelengero cha odwalabe pa 717.
Koma ngakhale chiwerengerochi chikutsika Ndunayi yalimbikitsa a Malawi kupitiliza kutsatilabe njira zopewera kufala kwa kachilombo ka Corona monga kusamba mmanja pafupi pafupi mwazina.
Chiponda walimbikitsaso anthu opyola dzaka 18 kukabayitsa katemera wa Oxford AstraZeneca yemwe amalimbana mliliwu.
Tithokoze omwe anapanga chisankho chobaitsa katemera ndikuonetsetsa kuti ali otetezeka.
Padakali pano tikugwiritsa ntchito Katemera wa AstraZeneca yemwe kuti umayenera kulandira kawiri pasabata 8 ndi 12 kuchokera tsiku lomwe unalandira.
Kamba ka izi gawo lachiwiri liyamba pa 03 June 2021.
Chiponda wanena kuti kufikila padakali pano anthu 332,995 ndiomwe alandira katemerayu.