Gides Chalamanda anabadwa pa 15 January m’chaka cha 1931. Kufikira lero, iye ali ndi zaka 90. Iye ndi wachinayi kubadwa m’banja la ana asanu ndi awiri (7).
Katswiriyu amachokera m’boma la Chiradzulu, Mfumu yaikulu Mpama, m’mudzi wotchedwa Madzuwa.
Gides sanapite patali ndi maphunziro ake chifukwa chosowa ndalama yolipira sukulu. Iye anasiira sukulu mu Sitandade 1.
Mavuto azachumawa anakula chifukwa bambo ake anathawa banja lawo n’kupita ku South Africa mu 1941,ali wachichepere. Izi zinachititsa kuti apite m’dziko la Zimbabwe kukagwira ntchito m’minda ya fodya.
Iye anayamba kuimba ali wachichepere. Ankagwiritsa ntchito banjo yomwe anakonza yekha. Atapita ku Zimbabwe, anakumana ndi anzake ena oimba omwe anali ochokera kuno monga Bali Paseli ndi Luka Malunga. Nyimbo yotchedwa Buffalo soldier imabweretsa maganizo osiyanasiyana: Gides anaimba nyimboyi m’chaka cha 1974 ndipo patapita zaka ziwiri(mu 1976) katswiri wotchedwa Bob Marley anaimbanso nyimbo yotchedwa Buffalo Soldier. Mu Buffalo Soldier ya Chalamanda, ankasilira kuona dziko la USA ndipo malotowa anakwaniritsidwa mu 2016 pomwe anapitako pamodzi ndi Edgar & Davis.
Chinthu china chochititsa chidwi n’chakuti Chalamanda anasewerapo nkhonya. Anasiya kusewera masewerowa atagonjetsedwa ndi chibagera chimodzi ndi katswiri wina wa m’dziko lomwe ankagwira ntchito(Zimbabwe).
Gides ali pabanja. Iye anakwatira Abiti Alfred wochokera m’boma la Chiradzulu lomwelo. Awiriwa anadalitsidwa ndi ana anayi(4). M’modzi wa anawa ndi Liny( wamkazi) yemwe anaimbidwa mu imodzi za nyimbo za Agide.
Infotainment Malawi ikungofunira zabwino zonse katswiriyu pomwe akupitiliza kusangalatsa anthu ngakhale wakalamba. Mulungu azimudalitsa.