Bwalo la milandu la Dowa First Grade Magistrate’s Lachitatu lagamula anthu asanu ndi awiri kuti alipire chindapusa cha K7000.00 aliyense kapena akakhale kundende mwezi umodzi kamba kophwanya malamulo a Covid-19.
Bwalo kudzera kwa woyimira boma pa milandu, Sub Inspector Ezara Bakili, lidamva kuti anthu olakwawo adamangidwa pa ntchito yosesa yomwe idachitika Lolemba ndi Lachiwiri sabata ino ku Dzaleka Refugee Camp ndi Dowa Boma chifukwa cholephera kuvala maski kumaso kuphwanya malamulo a Covid-19.
M’mawu ake, woimira boma pa milandu a Sub Inspector Ezara Bakili anachonderera bwaloli kuti lipereke chilango chokhwima kwa olakwawo ngati cholepheretsa anthu ena komanso kuti mliriwu usafalikire.
Popereka chigamulo, a First Grade Magistrate Amran Phiri adagwirizana ndi zomwe boma lidapereka ndipo adalamula kuti wopezeka ndi mlandu aliyense alipire chindapusa cha K7000.00 aliyense kapena akakhale kundende mwezi umodzi ndi ntchito yaukali kuti atumize ngati chenjezo kwa ena omwe akufuna kulakwa.