Mfumu yayikulu Chakhaza ya m’boma la Dowa akana ma desk omwe anagula Phungu wadela la kumpoto kwa Dowa ” Dowa north constituency” Enos Chitatanga. Izi zanenedwa pa mkumano wa maso ndi maso umene bungwe la CSAT linapanga ndipo mkumanowu unachitika pa Chakhaza CDSS.
Mfumu yayikulu Chakhaza ndi anthu ake anena Kuti Phungu wa nyumba ya malamuloyu akuyenera kubweza ma Desk amene anagula ponena Kuti ma desk amene anagulawo ndi osayenera sukulu ya sekondale, osakonzedwa mwa luso komanso ndi ochepa poyaluzila ndi ndalama zimene zinalipilidwa kwa kontalakitala zokwana K4,560,000.00 ndipo anagulidwa ma desk 25 okha mmalo mwa 100.Ndipo ndalama zikuchoka mu thumba la CDF mundondomeko ya chuma cha 2020 – 2021.
A Senior Chief Chakhaza apemphanso phunguyu kuti aphuzire kuchita zinthu poyera komanso kugwiritsa ntchito ma komiti achitukuko a ADC ndi VDC.
Mkuyankha kwake Phungu wa delali Enos Chitatanga anati iye wamvomera kukabweza ma desk kwa kontalakitala yemwe anapanga ma desk amenewa ndi kukagula ena atsopano. Phunguyu walonjeza kukwanilitsa zomwe walonjeza pa mkumanowu.
Mtola nkhani wa kumudzi anafuna kumva kuchoka kwa mkulu wa bungwe la CSAT Willie Kambwandira wati iye ndi osangalala Kuti phungu wadelali wavomera kuti agula ma desk ena ndipo amene anagulawo amubwezera kontalakitala amene anapanga ma desk amenewa. Koma mkulu wa CSAT anati nthawi yakwana tsopano yoti adindo aphuzire kuchita zinthu poyera ndi cholinga chofuna kupanga Malawi wabwino.
Mkulu wa mabungwe amene sali aboma ‘CSO network’ Fr Elias Chizule pamkumanowu apepha adindo kuti azigwilitsa tnchito makomiti azitukuko amene ali ku madera awo komanso azidziwa kuti mabungwe amene sali aboma amathandizira ntchito za boma ndipo ndipo ndi abwenzi pachitukuko.
Pa mkumanowu panalinso akuluakulu ena ochokera ku bungwe by lothana ndi ziphuphu ndi Katangale la ACB.