By Violet Thungula
Nkhani ya Silikali yemwe zidamveka kuti waphedwa pa msika wa Siyasiya, anthu okwiya atamumenya chifukwa chokuba ndalama za mkulu wina wochita malonda, ndalama zopyola K140,000.
.
Achibale a silikaliyu akuti nkhaniyi siyowona kuti m’bale waoyu waphedwa kokuba koma iwo akuti nkhani yonse inakhala motere;
Akuti Silikali ophedwayu ndizoti ali ndi a malume ake omwe ali ndi ng’ombe zambiri pa msika wa Siyasiya ndipo ng’ombe za malume akewa zakhala zikubedwa ndipo omwe amaganizilidwa kuti akumaba ng’ombe zimenezi, ndi anthu a pa Msika omweu wa Siyasiya.
Ndiye malume a malemuyu zitafika powatopesa, anamuwuza m’bale waoyu za anthu omwe akumusowesa mtendere kumamubera ng’ombe zake ndipo malumewo anapempha malemuyu kuti achitepo kanthu monga iye msilikali, amuthandize kuti mwina anthuwa asiye kumubera ng’ombe.
Ndiye akuti malemuyu (msilikali ophedwa), anapita pa Msika wa Siyasiya kukafufuza anthu omwe malume ake anamuwuza kuti akumaba ng’ombe zake…
Kafukufuku wa malemuyu ali mkati, anakumana ndi munthu modzi amene malume ake anamutchula dzina kuti ndiyemwe akumaba ng’ombe. Mkangano unabuka pakati pa malemuyo komanso oganizilidwayo.
Kenako oganizilidwayo ataona kuti wapanikizidwa komanso kusowesedwa mtendere pa malopo, anakuwa kuti “wakuba!! Wakuba!!”, Ndipo zitatero anthu anayamba kusonkhana pa malopo..
Malemuyo (msilikaliyo) anayesera kulongosola zomwe zimachitika pa malopo komanso kuwaziwisa anthuwo kuti iye ndi msilikali, koma zimenezi sizinaphule kanthu ndipo ataona kuti zinthu zikukulira kulira, iye anayamba kuthawa ndipo ali mkati mothawa, mwatsoka anakagwera mukazenje zomwe zinapangisa kuti abinye phanzi ndipo sanakwaniseso kuthawa.
Anthu anamugwira, ndipo ngakhale iye anapempha chifundo kwa anthuwo, sizinaphule kanthu.
Anthuwo anayamba kumumenya ndi miyala mpaka munthu kugonjeratu ndipo kenako anamuotcha.
Ku maliro a msilikaliyu, mwambo unayenda bwinobwino ndipo a mpingo wa Winners Chapel omwe malemuyu amasonkhana nawo boma la Salima, ndiwomwe anayendesa mwambo onse wa maliro.
Malemuyu pokhalanso kuti anali msilikali, chocho mtembo wake unalandiranso ulemu onse monga momwe zikhalira ndi maliro a chisilikali.
Zimenezi ndizomwe tauzidwa ndi achibale a malemuyu (msilikali ophedwa pa Siyasiya).