Sukulu ya ukachenjedwe ya Malawi University of Science and Technology (MUST) ayitseguliranso pa 29 March chaka chino
Malingana ndi chikalata chomwe akuluakulu asukuluyi atulutsa lolemba pa 7 Malichi chaka chino, chiganizochi chadza kutsatira nkumano omwe akuluakulu asukuluyi anachita pa 1 March chaka chino.
Chikalatachi chati ophunzira yekhayo yemwe anamaliza kulipira ndalama yophunzirira ku sukuluyi ndiye aloledwe kubwelera ku sukuluyi pa 26 March.
“Pamene sukuluyi tikutsegukiranso, tayika ndondomeko yoti ophunzira yekhayo amene analipira ndalama ya mayeso a chigawo cha chiwiri cha maphunziro am’chaka cha 2021/2022, ndiye adzaloledwe kulemba mayeso wa”, chikalatachi chatelo.
Sukulu ya MUST inatsekedwa pa 16 February chaka chino kutsatira zionetsero zomwe ophunzira apa sukuluyi anachita posagwilizana ndi ganizo la sukuluyi losalola ophunzira omwe sanamalize kulipira fees kulemba nawo mayeso.