Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera Lachinayi wavomereza Doha Programme of Action chifukwa ikufotokoza njira zothandizira mayiko osiyanasiyana pa zachuma, kuti achulukitse katundu ndi malonda m’mayiko osatukuka (LDCs).
Purezidenti walankhula izi ku Likulu la United Nations ku New York, pomwe amakamba nkhani yofunika kwambiri paudindo wake monga Wapampando wa Maiko Osatukuka povomereza Doha Programme of Action for LDCs.
Anati Doha Programme of Action imafuna kuyankha mogwirizana, pamodzi, komanso molimba mtima.
“Tiyenera kutengera Doha Program of Action, chifukwa ndi mwayi wathu wabwino kwambiri wokonza njira yopulumutsira mayiko omwe ali pachiwopsezo kwambiri padziko lapansi. Kuchitapo kanthu ndi chiyembekezo chathu, “adatero.
Chakwera adati Doha Programme of Action ndi yofunika chifukwa ndi Program yomwe cholinga chake ndi kusonyeza mgwirizano ndi mayiko osauka kwambiri padziko lapansi.
Anatinso poyambirira, mabungwe ndi zachuma zakhala zikuwunikiridwa ndi kusintha kwanyengo komanso zochitika zomwe zikuchitika motsatizana mwachangu kuposa kale.
“Dziko langa la Malawi likadali chimodzi modzi, chifukwa lidavulala kwambiri mu 2019 ndi Cyclones wa Idai ndi Kenneth, ndipo zilondazo sizinapole, tapezedwanso ndi mvula yamkuntho ya Ana ndi Gombe masabata asanu ndi awiri apitawa, kusiya chiwonongeko ndi imfa,” adatero.
Pamfundoyi adati Doha Programme of Action ndiye mwayi wabwino kwambiri wopangira njira yopulumutsira mayiko omwe ali pachiwopsezo kwambiri padziko lapansi.
Kupyolera mu madera asanu ndi limodzi omwe akuphatikizapo: kuthetsa umphawi, kulimbikitsa sayansi, luso lamakono ndi zatsopano komanso kuthana ndi kusintha kwa nyengo ndi mlili wa COVID-19, Doha Programme of Action ikufotokoza zomwe anthu apadziko lonse lapansi ndi LDCs akufuna kuti athandizidwe.