Timu ya Rumphi United yatuluka mu ligi yaikulu ya mdziko muno ya Tnm pamene yagonja pakhomo ndi timu ya Blue Eagles ndizigoli ziwiri kwa chilowele mumasewelo omwe anaseweledwa masana a lachisanu pabwalo la Rumphi.
Rumphi united imalowa mumasewelowa ikudziwa kuti kutaya ma points ena aliwose kuyitengera timuyi kuligi ya mchigawo chakumpoto ya Simso Inno build.
Kuyamba kwa masewelowa,timu ya Blue Eagles ndiyomwe ikanatha kupeza zigoli zochuluka koma kusagwilitsa bwino ntchito mipata ndikomwe kunapangitsa kuti isapeze chigoli Mu chigawo choyamba chomwe chinatha opanda mphatso yachigoli kumbali zose.
Kubwera muchigawo chachiwiri, Schumacher kuwali anatsogoza Nkhwazi zaku area 30 pa mphindi yachi nambala 5 ya chigawochi.
Posakasaka zigoli zozipulumutsila, timu ya Rumphi United inasintha pamene Edward Mkandawire komaso Aggrey Msowoya anatuluka ndipo mmalo mwake munalowa Christiano Muomba komaso Chimwemwe Kaliyala.
Nayo timu ya Blue Eagles inalowetsa Andrew Juvinala komaso Gilbert Chirwa m’malo mwa Stuart Mbunge ndi Ian Chinyama.
Pamphindi yachinambala 73, Gilbert Chirwa anagoletsa chigoli chachiwiri cha blue eagles chomweso chinali chinali chokwanila kuti timuyi itenge ma points onse atatu.
Kutsatila ndimomwe zayendera mu tsiku la lero,zatsimikizika kuti timu ya Rumphi United yatuluka mu ya TNM pamene timuyi tsopano ili ndima points 10 mumasewero 26 omwe yasewela ndipo ikusiyana ma points 15 ndi timu ya Red lions yomwe ili panambala 13.
Izi zikutanthauza kuti ngakhale timuyi itapambana masewelo ake ose omwe yatsala nawo singafikebe ma points 25.
Pamene kumbali yatimu ya Blue Eagles, tsopano yafika panambala yachiwiri ndipo yachepetsa mpata wama points kufika pa 7 ndi timu ya bullets.