Mabungwe komanso nthambi zomwe zili ndi upangiri pa nkhani za kaganizidwe kangwiro awapempha kuti ayambe kugwira ntchito ndi nthambi ya polisi pofuna kuthana ndi vuto la kuzipha.
Mkulu oyendetsa ntchito za polisi m’chigawo cha pakati, Dennis Banda, wanena izi ku Mchinji pa chikonzero chomwe amazindikiritsa anthu za chitetezo.
Banda wati ngakhale kuti padakali pano alibe chiwerengero chenicheni cha anthu omwe adzipha okha, komabe kuyang’anira kukhoza kupangitsa kuti chiwerengero cha anthu odzipha okha chikwere.
Komabe, iye walimbikitsa anthu kuti adzipita ku nthambi ya polisi yothandiza anthu pa zosiyanasiyana ya Victim Support Unit kuti alandire thandizo ngati ali ndi vuto lokhudza malingaliro.
Pa chikonzero-cho, mkulu wa polisi ya Mchinji, John Nkhoma, wati nkhani zodzipha, anthu kutengera lamulo m’manja mwawo komanso kuphana zikuchulukira m’bomalo.
Mfumu yaikulu Mavwere, yomwe-nso inali pa zokambirana-zo, inadandaula kuti anthu akudelera malangizo a atsogplero awo, zomwe zikubweretsa mavuto ena.