Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lati layimitsa kaye kufikira mtsogolo mikumano yomva maganizo a anthu pa pempho la kampani ya ESCOM lofuna kukweza mtengo wa magetsi mdziko muno.
Bungweli kudzera mu chikalata chomwe latulutsa lachisanu sabata ino lati silichita kaye mikumanoyi mu miyezi ya January ndi February chaka chino kutsatira kampani ya ESCOM yomwe yapempha kuti ilembenso zikalata zake zokhudza kukweza mitengo ya magetsi.
Bungwe la MERA lati pempho la ESCOM ladza kutsatira boma lomwe lathetsa mphamvu za kampani ya Power market limited zogulira magetsi ndikubwenzeretsa mphamvuzi ku Kampani ya ESCOM.
Mwezi wa August chaka cha 2022, makampani a ESCOM ndi Power market limited adati mu ndondomeko ya mitengo yatsopano ya magetsi ya zaka zinayi akufuna kukweza mitengo yogulitsira magetsiwa kuchoka pa K104 Kwh kufika pa K187.98 Kwh zomwe zikuyimilira 99 percent.