Wapampando wa bungwe loyendetsa chisankho a Chifundo kachalere ati zikalata zoponyera vote zifika mdziko muno pa 19 June ndipo iye wati company yomwe ikupanga zikalatazi yatsimikizira bungweli kuti ikhala itamaliza kupanga zikalata zosaposera 6.9 million mu matsiku 7 ndipo pofika pa 19 akhala atazitumiza ku Malawi kuno.
Nkhaniyi yabweretsa chimwemwe komanso kuchotsa nkhawa amalawi omwe amakaika kuti zikalatazi zichedwa.
Mmene zililimu ndekuti pa 20 bungwe la MEC lizayamba kugawa zikalatazi kuti zifikire mmadera onse , izitu zikuthandauza kuti campaign izatha pakati pa 20 ndi 21 June
MEC kutsogozedwa ndi chair watsopano wati akuchita zinthu mwa changu kuti akwanilitse chigamulo Cha court