Mkulu wa bungwe lothana ndi Katangale la Anti Corruption Bureau (ACB), Reyneck Matemba, apempha bwalo la milandu la Blantyre Chief
Residents Magistrate kuti lipititse ku bwalo la milandu la High Court, mlandu wokhuza mkulu wa FDH Bank, a Thom Mpinganjira.
A Thom Mpinganjira akuganizilidwa kuti ankafuna kupereka ndalama ya chiphuphu yokwana MK100 miliyoni kwa anthu omwe ankaweluza mlandu wokhuza chisankho chapa 21 May 2019 ndi cholinga choti anthu oweruza mlanduwo apereke chigamulo chokomera Prof Peter Muntharika ndi bungwe la MEC kuti m’dziko muno musachitike chisankho chachibwereza cha pulezidenti.