Bungwe lomenyera ufulu wa achinyamata mdziko muno la Youth Freedom and Democracy (YFD) lifuna kuti Joyce Banda, Dr Chakwera komanso gulu la HRDC lipepese Ku mtundu wa aMalawi.
Bungwe la YFD likufuna kuti Joyce Banda apepese ku mtundu wa aMalawi maka ponamiza aMalawi kuti mdziko muno mulibe Corona virus.
Mkulu wa pa mpando wa bungweli Alex Black Moses yemwe amadziwika ndi dzina loti Black-more, wati akufuna kuti Joyce Banda komaso Dr Chakwera apepese ku mtundu wa aMalawi maka ponamiza anthu mdziko muno kuti mulibe Corona virus zomwe ati zinayika miyoyo ya aMalawi pachiwopsyezo kamba koti anthu ambiri anamvela zonena za achina JB ndi Chakwera zija.
Bungwe la YFD lati Dr Chakwera komanso JB ndi amene adaika miyoyo ya aMalawi pachiwopsyezo kamba kofuna voti. BungweAli lati anthu a ndale mdziko muno ayenera kudziwa kuti moyo wa munthu ndi moyo ofunikira kwambiri kuyerekeza ndi voti.
Masiku apitawo Joyce Banda mosogozedwa ndi Dr Chakwera anabwera poyera ndikuuza anthu mdziko muno kuti Ku malawi kuno kulibe Corona virus; dziko la Malawi mulungu amalikonda kwambiri motere kuno Ku Malawi kulibe Corona virus.
Gulu la HRDC lidapita ku court kukatenga chiletso choletsa kuti mdziko muno mukhale m’bindikiro (lockdown). YFD yati HRDC naye ili m’gulu loyika miyoyo ya aMalawi pachiwopsyezo kamba kokana lockdown, zimene zikanathandiza kwambiri.
YFD yati ikudziwa komanso ili ndi umboni onse kuti gulu la HRDC limene lija si bungwe lomenyera ufulu wa anthu kamba koti zimene amapanga si kumenyera ufulu wa anthu koma kumenyera ufulu wa zipani.
Bungwe la YFD lati ngakhale zili choncho nawo ayenera kudziwa kuti moyo wa munthu ndi moyo wofunikira kwambiri kuyerekeza ndi ndale.
Bungweli lapereka masiku asano ndi awiri (7) kuti anthuwo apepese ku mtundu wa aMalawi. Kulephela apo, alembera kalata Ku bungwe la za umoyo padziko lonse la WHO ndi ICC kamba kozawerengera miyoyo ya aMalawi.
Bungwe la YFD lati silingapangise mademo kamba koti mdziko muno muli covid-19. Koma bungweli lilembera kalata ku bungwe la WHO komanso akamang’ara ku ICC