Police Update
Apolisi m’boma la Dedza amanga bambo wa zaka 47 yemwe dzina lake ndi Levison Manyozo pa mlandu woganizilidwa kuti wakhala akugwililira/ akugonana ndi atsikana achichepere okwana 7.
.
Malingana ndi m’neneri wa apolisi ku Dedza a Sub inspector Edward Kabango wati atsikanawo ndi a zaka zapakati pa 8 ndi 11, wamkuluko ali kalasi ya Std 3 pomwe wang’onoko ali kalasi ya Std 1.
.
Atsikanawo akhala akugonedwa ndi bamboyo pa nthawi zosiyana siyana komanso malo osiyana.
Bamboyo ali ndi Shop m’mudzi momwe amagulitsamo zinthu zosiyana siyana ndipo bamboyo wakhala akumanyengerera atsikana achichepere pomagonana nawo pomawapatsa ma sweets ndima biscuits.
.
Pa 2 July 2020 atsikana ena amasewera pomwe bamboyo amkadutsa ndipo tsikana wina anawulula kwa mzake kuti wakhala akugonana ndi bamboyo kuchokera chaka chatha ndipo amapatsidwa zakudya monga ma sweets ndi biscuits, tsikana winanso nayenso anamuwuza mzakeyo kuti iyeyonso amagonana ndi bamboyo, pomwe anawo/ atsikanawo amakambilana izi pamadutsa munthu wina Wamkulu yemwe amamvetsera mwachidwi zokambilana za atsikanawo mpakana munthuyo anakanena nkhaniyi kwa makolo a atsikanawo. Zotsatira zaku chipatala cha boma la Dedza zinatsimikizadi kuti atsikanawo akhala akugonedwa/ kugwiliridwa ndi munthu wa bambo.
.
Bamboyo amachokera m’mudzi mwa Mkumayani T/A Kasumbu m’boma la Dedza ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku khothi lero kukayankha mlandu wogwililira kamba koti kugonana ndi mwana wosakwana zaka 18 ndi chimodzimodzi kugwililira malingana ndi malamulo.