Nduna za boma zomwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera anasakha, tsopano lero zalumbilitsidwa mu mzinda wa Lilongwe ku BICC ndipo Chakwera wanena kuti sasitha anthu omwe wawasakha kukhala nduna ngakhale kuti ena mwa ndunazo ndi apa chibale/ ochokera ku banja limodzi.
Chakwera wakana kusitha m’ndandanda wa nduna za boma lake ngakhale kuti anthu wochuluka mdziko la Malawi amadandawula kuti kuli mabanja ena komwe kukuchokera nduna ziwiri/ zitatu, Chakwera wanena kuti ngakhale nduna zina zili zochokera ku banja limodzi komabe iyeyo Chakwera sanasakhe anthuwo kutengera kuma banja komwe amachokerako koma iyeyo Chakwera wasakha ndunazo kutengera kuthekera kwake kwa ndunazo komanso ndunazo zili ndi zoziyenereza kukhala nduna.
Iye wanena kuti pa miyezi isanu (5) akhala akuziwunika ndunazi malingana ndi m’mene zikugwilira ntchito kapena kuti zikhala pa Probation ma unduna ndipo nduna zomwe zalephera kugwila bwino ntchito adzazichotsa pa udindo komabe iye wati atha kuchotsa nduna iliyonse pa udindo mu nthawi iliyonse ngati ndunayo ikukanika kugwila bwino ntchito.
Mtsogoleri yu wanena kuti anthu asadandawule Chifukwa cha kusowa kwa unduna wowona zoti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo komanso unduna wowona za anthu a ulumali, Chakwera wati ntchito zama undunawo pakadali panopa zayikidwa pansi pama unduna ena omwe wasakha iyeyo.
wati mkati mwa miyezi isanu, akhala atayika azimayi pama udindo akulu akulu ama unduna.
wafotokozanso kuti iyeyo ndi pulezidenti woyamba kuno ku Malawi kukhala ndi chiwerengero chochuluka Cha nduna za boma zomwe ali azimayi.