Osewela wakale wa Flames komanso Nyasa Big Bullets Fischer Kondowe wati ali ndi mafunso opanda mayankho maka mmene team ya Flames yachitila masewelo ake a friendly Zambia komanso Zimbabwe lamulungu lapitali.
Polankhula za ma games awiliwa Fischer wati kuzipeleka ndikomwe kukuvuta kwa anyamata athu a flames iye anati anyamatawa akuoneka kuti sali okonzeka kuvala makaka a Flames.
Kondowe wati anali okhumudwa kuona mmene osewela amalephelela kugoletsa komanso kupeleka mipila yabwino anong’a anati coach ali ndi ntchito yaikulu kuwauza osewela zoyenela kuchita akafika m’box watelo Anon’a.