Mosiyana ndi zomwe Unduna wa Maphunziro walengeza dzulo kuti Aphunzitsi abwerere Ku ntchito, palibe sukulu yaboma iliyonse yomwe ana ukuphunzira.
Mbali ziwirizi pakati pa boma ndi aphunzitsi zikulephera kumvana pa nkhani ya ndalama za Ukadziotche malingana ndi Mlili wa Corona Virus.
Mu chikalata chomwe Unduna wa Maphunziro unatulutsa , chinafotokoza kuti magulu awiriwa anali ndi nkumano omwe amakambirana madandaulo onse ndipo pa nkhani ya Risk Allowances yaponyedwa Ku nthambi yomwe ikuona za Covid 19, izi zili malingana ndi Mlembi Wamkulu Ku Undunawu a Kiswel Dakamau.
A Dakamau anatiso Ku mkumanowo anakambiranaso zokhazikitsa Khonsolo ya Aphunzitsi yomwe cholinga chake ndikupereka madandaulo awo mwa Luso komaso kuonetsetsa kuti zinthu za Umoyo wabwino zkuchitika.
Koma a Willy Mwalimba yemwe ndi Nkulu wagulu la Aphunzitsi [TUM] anapituliza kumemabe Aphunzitsi kuti lero pa 01 March asapezeke pa ntchito pomwe ati boma laonetsa usalabada kamba kamba koti zonsezi ukunena Unduna wa Maphunziro sanakambirabe nawo.
Izi zabweretsa kusamvana mkati kati mwa TUM pakati pa a Mwalimba komaso owatsatira awo pa u Udindo a Rehema Harid omwe analengeza kuti Aphunzitsi ayambe ntchito poti gulu lawo lachita zokambirana ndi boma kuphatikizaposo gulu la ‘Aphunzitsi Okhudzidwa motsogozedwa ndi a Harry Kamwaza apa sukulu ya Mchinji Secondary school anakamba chimodzimodzi.
Ndipo mmalo mwake wamkulu wa gulu la’Aphunzitsi Okhudzidwa Azeez J Losa aophseza kuchita zionetsero ngati Rehema Harid, Enerst Chirwa , Elistina Chizungu , Elton Chaulura komaso Newton Chafukira ngati Satula pansi ma Udindo omwe amatenga Ku gulu la TUM kamba kopweteketsa aphunzitsi anzawo. Iwo anatiso ndi President wa TUM yekha yemwe ali ndi mphamvu zolamula Strike kutha osati
wina wapadera.
Ndipo padakali pano magulu awiriwa TUM ndi Boma akuyembekezereka kukumana pomwe akambirane za chitsogolo cha kusamvanaku.
[Zinthunzi : Mphande Primary ndi Secondary school komaso Dzeyo Primary school m’boma la Mwanza ndi ina m’boma la Chikwawa]