Bungwe la Malawi Revenue Authority (MRA) lati lathamangitsa antchito ake khumi ndi atatu mchaka cha chuma cha 2020/2021 kuti ena atengerepo phunziro pantchito yawo yosonkhetsa misonkho kwa a Malawi.
Ogwira ntchito wa akuganizilidwa kuti amaba ndalama kwa nzika pantchito zomwe samayenera kulipira misonko.
Mkulu Woyang’anira Bungweli a Steven Kapoloma wati ziphuphu zachuluka chifukwa nzika zina za Malawi sizidziwa njira zina zokhudzana ndi misonkho.
adatinso akudziwa anthu ochepa omwe akuipitsa mbiri ya ulamulirowu wa boma lino chifukwa cha zizolowezi zawo zoyipa zomwe zimakhumudwitsa omwe amapereka misonkho omwe amasiya kukhulupirira olamulira.
“Ena mwa omwe adachotsedwa ntchito akuganizilidwa kuti amapempha ndalama kwa anthu pazinthu zomwe sayenera kulipira, kugwiritsa ntchito mwayi wosazindikira momwe MRA imagwirira ntchito,” adalongosola a Kapoloma.
MRA yati yayamba kulumikizana ndi omwe amapereka misonkho kuti amvetsetse kufunikira kokhoma misonkho.
Bungweli lidapatsidwa ntchito yosonkhanitsa K1.079 trilioni mchaka chachuma cha 2020/21 koma lidakwanitsa kupeza K28.7 biliyoni yowonjezera. Adapatsidwa ntchito yosonkhanitsa K1.033 trilioni mchaka chachuma cha 2021/2022.