Bungwe la Returnees and Ex-Detainees Association of Malawi lakana kwamtu wagalu kuti akufuna ndalama zokwana 23 trillion Malawi kwacha ngati chipepeso kuchoka Ku chipani cha Malawi Congress Party (MCP) ati kaamba kankhaza zomwe adakumana nazo munthawi ya ulamuliro wachipani chimodzi m’dziko muno.
Bungweli lachititsa msonkhano wa olemba nkhani lero mum’zinda wa Lilongwe kutsutsa kalata yochokera kwa mulangizi wamkulu waboma pankhani zamilandu Thabo Chakaka Nyirenda yomwe inatuluka masiku apitawa ndipo kalatayi imati gululi likufuna ndalama zokwana 23 Trillion Malawi kwacha.
Lyson Betha yemwe ndi wachiwiri kwa wapampando wabungweri wati Iwo ndalama zomwe akufuna ndizoyambira MK600,000 malire MK20,000,000 munthu m’modzi.
Betha wati ndiodabwa kwambiri zokhudza nkhani-yi kaamba koti iwo sadakumanepo ndi mulangizi wabomayu ndikukamba nkhawa zawo.
Anthu omwe ali mugululi amanena kuti adakumana ndi nkhaza zosiyanasiyana muulamuliro wa chipani chimodzi cha MCP kuchoka chaka cha 1964 mpaka 1994.