Apolisi mu boma la Karonga akusunga nzika za ku Ethiopia 72 zimene chifukwa cholowa mdzika muno opanda chilolezo komanso ziphatso
Mneneli wa polisi George Mulewa watsimikiza za nkhaniyi kunena kuti anthuwa apezeka mu nkhalango ya Vithukutu Ku Chirumba ku Karonga.
Mulewa wati adatsinidwa khutu ndi anthu ena akufuna kwabwino za anthuwa ndipo Iwo mogwirizana ndi asilikali aku Chirumba Barracks analowa mkhalangomo nkukawapeza.
Malinga ndi a polisi, anthuwa amadikira anthu amene akuganizilidwa kuti ndi nzika za Malawi kuti akawatenge adzipita nawo ma dera ena ndipo Iwo agwiraponso nzika za Malawi Khumi poziganizira kuti ndizomwe zimathandiza anthuwa.
Kutsatira izi, apolisi akuchejeza a amalawi onse kuti asamapange mchitidwe umenewu chifukwa zitha kubweretsa mavuto akulu kuchitetezo Cha dziko komanso matenda.
Kupezeka Kwa anthu 72 mu nkhalango ya Vithukutu Ku Karonga kwachitika patangodutsa tsiku limodzi ku nkhalango ya mtangatanga boma la Mzimba kutapezeka mitembo ya anthu 25 itakwililidwa mu dzenje limodzi.