Bwanankubwa wa boma la Lilongwe Lawford Palani wapeleka chilolezo kwa gulu la omenyera ufulu omwe akufuna kuchita zionetsero sabata ya mawa
Kudzera mu kalata yomwe bwanankubwayi walemba yapempha ochita zionetserowa kuti adzasunge bata, asadzanyamule zida komanso adzavale moyenerera
Komabe, a Palani auza anthuwa kuti kalata yomwe akufuna kukapeleka kwa mtsogoleli wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera, idzapelekedwe kwa iwowa
Izi zikusemphana ndi zomwe gululi linapempha kuti likasiye kalatayi ku nyumba ya chimfumu ya mtsogoleli wa dziko lino
Mu gululi muli atsogoleli monga a Joshua Chisa Mbele, Silvester Namiwa, Bon Kalindo komanso a Phunziro Mvula
Zionetserozi zikuyenera kuchitika lachisanu lino pa 28 October.