Ophunzira pa sukulu ya Primary ya Mphanda ku Nkhoma m’boma la Lilongwe apha ndikuotcha ndi moto thupi la munthu wina yemwe amamuganizira kuti ndi wakuba.
M’neneri wapolisi ya Lilongwe, Inspector Hastings Chigalu wati izi zachitika lolemba sabata ino m’dera la mfumu yaikulu Chitekwere ndipo malemuyu ndi Masautso Felison wazaka 31 ochokera m’mudzi mwa Kadzidzi, mfumu yaikulu Mazengera m’bomalo.
Chigalu wati malemu Felison akuganizilidwa kuti adaba katundu osiyanasiyana pasukulu ya Mphanda monga mipando 13, batile la Sola komanso inverter.
Ndipo patsikulo anthu am’mudzi anamugwira oganizilidwayu pomwe amapita naye kupolisi unit ya Nkhoma podzera panjira yapasukuluyi.
“Ndipo ophunzira pasukuluyi atazindikira kuti oganilidwayu akutengedwera kupolisi adawalanda anthu am’mudzi ndikuyamba kumumenya komanso kumugenda ndipo atafa thupi lake analiotcha ndi moto,” watelo Chigalu.
Iye wati zotsatira zachipatala cha Mtenthera zidaonetsa kuti malemu Felison wamwalira kaamba ka kuvulala kwambiri m’mutu kutsatira kumenyedwa.
Apa Chigalu wachenjeza kuti kutengela lamulo m’manja ndikolakwika pamalamulo a dziko lino ndipo yense opezeka olakwa pamlanduwu azalandira chilango